Pempho langa kuno ku Machinjiri ndi lakuti atikonzere miseu ingapo monga wochoka pa Khama to Chikoti market
Miseu yaonongeka maka Ku nandolo ndi Ku mboni.
Ife kuno kuchilomoni kwa nthukwa tufuna atikonzere msika wathu kuti ukhale wabwino
I would like to express appreciation to Blantyre City Council for the street lights project, way to go.
There is so much trash around the area close to Golden Peacock Hotel. Trash is dumped in drums and on the ground and we are not sure on who is responsible but the place is smelling and it is hazardous to health
Pa Makhetha clinic tati tipemphe nawo kuti atikonzere ma Toilet, anadilizika
Am a young man living here in Bangwe.My concern is the lack of sufficient health personnel at Bangwe health center. I also would like to say I am one of the youth who has the willingness to work with our leaders towards development. Let them contact us.
Tilibe Bin pa Msika kuno ku Makata ward ku Ndirande, kotero anthu amatenga zinyalala kukataya mu mtsinje wa Nasolo. izi zimaika miyoyo ya anthu pa chiophyezo chifukwa ena amamwa madzi omwewa
Kuno ku mamiyango vuto ndi madzi ndi magetsi komanso miseu silibwino
Kuno kwa Kachere tati tipemphe kwa a-Water Users Association kudzera mwa Blantyre Water Board kuti apange chotheka kiosk ya m'mudzi mwa Andulu iyambenso kugwira ntchito. Ine Cosmas Chamveka
Ndati ndiyamikire khansala Mike Chimzukira wa Mbidzi ward popanga dongosolo la ma bin otayiramo zinyalala mu malo osiyanasiyana. Izi zikulimbikitsa ukhondo.
Kuno ku Mbayani limodzi mwa mavuto omwe tili nawo ndi kusiyasiya kwa madzi. Ndine Maggie Chirwa
Ndati ndikambe nawo kuti kuno kwa Kachere madera ena madzi amasiya nthawi yaitali pamene kwina kwa kanthawi kochepa. kodi ichi ndichifukwa chani
Ndati ndipemphe nawo kudzera mwa Khansala wathu kuti mseu wochoka pa Khama to miseu 6 sulibwino. Atiganizire pa malingaliro awo achitukuko mtsogolo muno
Pa Msika wa Kachere chi Bin cha zinyalala cha dzadza, chonde abwere azachotse