Pempho Pa Za Mlatho Wa Pa Mlombozi

28-Mar-2017 | 11:34

Kuno ku Makata Blantyre mlatho wa pa mtsinje wa Mlombozi suli bwino udaonongeka ndi mvula. Uthenga tidaufikitsa kale kwa atsogoleri ndipo tikukhulupilira kuti ngakhale iwo eni ake akudziwa koma sitidamveko ndi lonjezo limene loti achitapo kanthu

Pa Msika Wa Mboni Kwa Mtsiliza Palibe Zimbudzi

28-Mar-2017 | 05:21

Kuno kwa Mtsiliza pa msika wathu wa Mboni palibe zimbudzi.

Faulty Transformer *RESOLVED*

27-Mar-2017 | 13:12

Here in New Naperi there were sparks at the transformer at the corner where roads from Joy radio and Havana's intersect. Currently there is no power.

Dandaulo pa kakonzedwe ka mseu

27-Mar-2017 | 10:57

Ine m'malo mwa anzanga ena kuno kwa Senti tili osakhutira ndi m'mene nseu waukulu kuno wakonzedwera. Mbali zina zomwe amaliza kale kukonza kuno zayamba kale ma pothole sitikudziwa kuti kodi ndi ukatswiri omwe unachepa kapena material sidali yokwanira

NOTICE FROM BWB

17-Mar-2017 | 18:17

Technicians are still working on a 450mm pipe burst fault in Kwacha Central Area. Therefore, Chinyonga, Kanjedza and other areas in Limbe will continue to experience no water until the problem is resolved. We will keep you updated.

Pempho pa nkhani ya chitetezo ku Area 36

17-Mar-2017 | 17:28

Kuno ku Area 36 m’maka ma dera akwa Zapita ndi Kandikole umbava ukuchuluka. Tipemphe atsogoleri athu alinganize ndi a community police achitepo kanthu

Chinsapo 2 atikonzere nsewu

17-Mar-2017 | 15:27

Kuno kwa Chinsapo 2 tingasangalare atatikonzera nsewu wochoko pa Chinangwa kupita pa sukulu ya Kakule primary

Pempho la Bin pa msika wa Mbayani

17-Mar-2017 | 15:26

Tati tipempheko kudzera mwa Khansala wathu kuno ku Mbayani kuti tikufuna Bin yaikulu yotayamo zinyala chifukwa anthu akumataya zinyalala ku njanji ndipo izi zikubweretsa mphepo yoyipa kwa anthu okhala nyumba zakufupi ndi kumalowa.

Nkhani ya ukhondo ku Kawale 1

17-Mar-2017 | 15:23

Ndati ndipempheko atsogoleri athu kuti akambirane ndi akuluakulu apa Kawale health centre kuti pakhale njira yowonetsetsa kuti anthu sakutaya zinyala paseli pa chipatalachi. Kuunjikana kwa zinyalala pamalopa kukuika miyoyo ya ana athu pachiophyezo chifukwa ena amapita kukasewerapo

Pempho la wáter kiosk ku Ndirande Zambia

17-Mar-2017 | 15:09

Ndati ndipemphe kuti ife kuno ku Ndirande Zambia timasilira anzathu ku Makata ali ndi wáter kiosk yabwino pa Khoza pamene ife kuno kulibe. Kodi mabungwe omwe adathandizapo za Project imeneyi kuno sangafike?

Kuvuta kwa madzi ku Machinjiri

17-Mar-2017 | 14:10

Kuno ku Machinjiri kwa Mkwate madzi akusiyasiya kulekana ndi madera ena ku Machinjiri konkuno, kodi ichi ndi chifukwa chachani

Vuto la kuzima kwa Magetsi kwa Mtsiliza

17-Mar-2017 | 13:21

Kuno kwa Mtsiliza vuto la kuzima kwa magetsi likupitilira kodi zinthu zizasintha liti

Appreciation to Lilongwe City Council

17-Mar-2017 | 12:20

Let me commend Lilongwe City Council for stepping up efforts to keep the city clean.

Tikupempha ma Toilet pa nsika ku Kaliyeka

17-Mar-2017 | 08:19

Pansika wa Kaliyeka ma toilet palibe ngati kuli kotheka atiganizire chifukwa nkhani ya ukhondo sili bwino.

A Message from the Mayor of Lilongwe City

12-Mar-2017 | 13:34

LILONGWE REFUSES REFUSE Moving around Lilongwe you are greeted by a strong unpleasant smell from huge refuse piling up, especially around market areas - Area 25 Nsungwi, Area 18, Kawale, Chilinde, Area 23, Area 36, just to mention a few. I am glad to indicate that we have engaged PVHO who have already started clearing refuse from these strategic areas as a short-term measure to arrest the situation while we work on addressing Council refuse collection challenges. We have started off with Area 23 then will move to Kawale, Area 36, Falls, and so on. It is pleasing to declare that Chilinde is now 100% clean. This development is inline with my 10 Point Plan, especially within the scope of improving refuse collection and waste management

On foot-pass bridges in Limbe

12-Mar-2017 | 06:49

I wish to reach out to the Councilor for Limbe ward to take the initiative to undertake maintenance work on the foot-pass bridges that connect Limbe market to the upper area where there are shops.