A Big-up to our Councilor for taking the initiative to raise awareness on the need to keep Lilongwe clean. I believe among ourselves if this is taken heed of sitizionanso kutaya kwa zinyalala paliponse kumalo ngati ku Depot.
I would like to report about sanitation regarding mzuzu healthy centre adjacent to shoprite, cotton wools and other disposables are being dumped any how. We are engaging the adminstration officer today but would be happy if the city council intervened
Kuno kwa Biwi osesa ndi kuola zinyalala mu nseu achilimike.
kuno kwa cent kumsika kulibe bin yotailamo zinyalala moti anthu amangotaila pena paliponse zinyalala. Atipatse Bin
munsika mulibe toilet kuno ku Kaliyeka
Kuno ku Mchesi ngati kuli kotheka chi galimoto chotenga zinyalala chizidutsa kawiri. kanthawi komwe sichikudutsa ukhondo siukutheka
Kuno Kulilongwe Ku Area 25 tithokoze atsogoleri athu potengapo danga kuti dera likhale la ukhondo polamula kuti azapezeke akutaya zinyalala paseli pa Rank azalipira
Kuno ku Lumbadzi pa Msika Bin palibe, izi zupereka chiophezyo cha matenda kamba kosowa ukhondo
Ndine joyce chisale ndikuchokera mumzinda wakwa mtsiliza vuto kuno chigalimoto chowola zinyalala sichifika
Ndine Shukuran Mtadile Market ikufunika kukonza ma toilet
Msika wathu wa Mboni ulibe madzi komanso ma Toilet
Ndati ndinenepo kuti Kusoweka kwa ukhondo mu madera athu pena nchifukwa choti ife anthu eni ake sitifuna kutengapo mbali. Sinkhani yomangonena kuti City council sikuchitapo kanthu.