LLCH 1 Kuno ku Chigwirizano market pempho lathu ndi lakuti azachose dzala pomwe tikutayapo pano likupereka chiophyezo cha matenda. Lisunthire pena olo atipase Bin yaikulu
Pa msika wa Mathambi pakuchepa anthu osesa. Panopa alipo mmodzi yekha ndipo lero wadwala kotero sabata yonseyi simunasesedwe.
Chilobwe market pano patha ma sabata awiri osesa mu msika akukhonsolo asakusesa chonsecho ndalama yapangira malonda mu msika akutidula
Kuno ku Area 24 pafupi ndi panyenye stage pipe ya madzi ya water board yaphulika
Kuno ku Kafukule miseu yobwera pa msika waukulu sili bwino akonze ngati kuchoka kwa Chuyu, chinyera ndi mphimbi
Tafuna kukudziwitsani Kuti Kuno Kwa Ta Masumbankhunda Chimanga chikuoneka kuti chiuma ndi ng'amba kuyambila Phililanjuzi Mkoko Mabwela Sinyala Yemba Kalonga Chibudu ndi Kamphinda zikanakhala bwino ma Bungwe ndi Aboma kudziwonela okha gati momwe achitila ku Mangochi Ine Noel Batizani. Malingunde
Kuno ku Mulanje Mimosa. Pempho ndi loti atipalire mseu kuchoka pa Mimosa kufika pa msika wa Chikuse. Mayendedwe monga kwa anthu ochoka kwa Nkhonya amavutika.
Our transformer here in Area 25 B close to pa Chi ntengo has developed a fault and we have not had power since morning
Ku nkhani ya maphunziro kuno kwa chiuzira ku Lilongwe, dandaulo lathu ndilakuti pa school pali ana ambiri pamene ma block ndi ochepa zomwe zimapangitsa kukhala ana oposa 100 mu class imodzi zomwe zingapangitse kupatsirana matenda odzera mu mpweya komanso kovuta kwa ena kuti aphunzire bwino
pa msundwe market palibe ma toilet okwanira
I just sent a report from Baghdad, Chimdidi Street. We have a fault. All of the other houses have electricity except ours and the neighbour that we share a poll
Ine ndati ndipempheko ku khonsolo kuti itikonzere ti migula kapena kuti ngalande zodutsamo madzi pa msika wa Malingunde. Atatikonderanso nkumanga ma shade zingakhale bwino
Kuno ku Lilongwe ku Msinja tati tipemphe nawo kuti atikonzere mlatho pa Malili, madzi akumadzadza nkupangisa kuti msewu usatheke kudutsika mvula ikagwa yambiri