Mjigo Unaonongeka Kalekale Kuno Ku 24 Sector 2 Ndipo Khansala Wathu Ndi Elijah Botha Chonde uthenga uwafike atithandize,ine Munthu Wamba Sparrow Kadeka
Ine Milaji kwa mtsiliza kumboni. kodi nchifukwa ninji kuno kulibe ti ma bank ta madzi pamene kwa anzathu ngati kwa chinsapo aliko?
munsika mulibe toilet kuno ku Kaliyeka
Mutikozeleko Nseu ku 49 wochoka pa Zebra stage kulowa nkati kupita pa Mvama Church
Kuno Kulilongwe Ku Area 25 tithokoze atsogoleri athu potengapo danga kuti dera likhale la ukhondo polamula kuti azapezeke akutaya zinyalala paseli pa Rank azalipira
Kuno kwa Senti project yomanga nseu ikuchedwa chifukwa cha ndale
Vuto lina tili nalo ku Mtandile ndikuchepa kwa Chitetezo. Atipatse Police Unit ngati kuli kotheka. Felix Chikopa
Msika wathu wa Mboni ulibe madzi komanso ma Toilet
Ndine joyce chisale ndikuchokera mumzinda wakwa mtsiliza vuto kuno chigalimoto chowola zinyalala sichifika
ndine joe malenga kuno ku mtandile vuto lathu ndi la chipatala chili kutali
Ndine Shukuran Mtadile Market ikufunika kukonza ma toilet
Kuno ku mtandile timakumana ndi mavuto akusowa kwamadzi,magetsi,misewu yamakono,police unit.
Ndine Joe Malenga kuno kwathu ku Mtandile tilibe ka chipatala ka boma ngati ka health centre kapafupi
Kuno kwa Senti tikupempha kudzera mwa Khansala wathu kuti atikonzere mlatho wopita pa Mkombaphala
Ndati ndinenepo kuti Kusoweka kwa ukhondo mu madera athu pena nchifukwa choti ife anthu eni ake sitifuna kutengapo mbali. Sinkhani yomangonena kuti City council sikuchitapo kanthu.
Kuno kwa Mtsiliza tiyamike dongosolo loika ma ring mu miseu koma pakufunika madera onse zitheke nthawi ya mvula isadafike