Some street lights along the Ndirande magalasi road are not working. Would they please rectify
A khansala a LL city west zimene anatilonjeza nthawi ya kampeni sanayambe kupanga ndiye apanga liti popeza nthawi ikutha
Kuno ku lilongwe north constituency akhansala athu Bambo Kazamira ati sadadziwitsidwe za Mzinda. Tsono tikatuma uthenga atithandiza bwanji?
Committee ya chitukuko ya mtsiliza ward sinalandile maphuziro am'mene ingagwirile ntchito yake. tilowele kuti,kuti anthu awa akhale ndi knowledge pam'mene angapangire dongosolo mukulumikizana ndi anthu kuti chitukuko chiyende
our team will urgently rectify the faulty lights
kuno ku Tsabango 2 kwavuta nkhani ya ma block leade. zikuoneka kuti khansala wathu ankafuna munthu wina ku Benito ndipo adawina ndiwina kotero akulephera kugwira naye ncthito. pakuchitika ziwawa
Kodi Mzinda sungafikilenso m'maboma? ine B Sichinga ku Karonga
Amene mukupanga za Mzinda chonde pamene mukutilumikiza ndi atsogoleri komanso ama Bungwe musalowetse ndale likhale loyima palokha Nadine T S Banda. kwa Kauma
kuno ku maDisi ku dowa kuli njala. atithandize ndine chipangano kabwinja, madisi,in dowa, TA.Achakhaza
kuno Ku area 23 tsabango 1 palivuto lakusanvana pakati pa khasala ndi mafumu monga adaudi and astand akhasala amadana ndi imodzi mwa mafumuwa zimenezi sizabwino
Ndati ndipempheko kuti ngati kuli kotheka mabungwe omwe mukupanga za Mzinda mutifikireko ife akumadera ena monga kuno ku Matawale
Kuno ku Mtandire kwayamba mapokoso pankhani ya Admarc, pamalo pomwe akufuna kuyika akhansala, Azimayi amagwirapo ntchito yosamala ana amasiye. Chonde amabungwe iwafikire nkhaniyi alowererepo kuonetsetsa kuti zokhumba zandale zisasokoneze njira zina zomwe ena akuthandizikira kudera